Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 15:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.

2. Nthambi iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka.

3. Mwakhala okonzeka tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu,

4. Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.

5. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kucita kanthu.

6. Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.

7. Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu.

8. Mwa ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.

9. Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'cikondi canga.

10. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'cikondi canga; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'cikondi cace.

Werengani mutu wathunthu Yohane 15