Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 14:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace.

5. Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji?

6. Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

7. Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye.

8. Filipo ananena ndi iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira.

9. Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?

10. Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace.

11. Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe.

Werengani mutu wathunthu Yohane 14