Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 14:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?

23. Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.

24. Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo 1 mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.

25. Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.

26. Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

27. 4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.

28. Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, 6 Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; 7 pakuti Atate ali wamkuru ndi Ine.

29. Ndipo tsopano 8 ndakuuzani cisanacitike, kuti pamene citacitika mukakhulupire.

30. Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti 9 mkuru wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;

31. koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndikuti 10 ndicita monga momwe Atate wandilamulira. Nyamukani, tizimuka kucokera kuno.

Werengani mutu wathunthu Yohane 14