Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 14:17-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.

18. Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu.

19. Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.

20. Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.

21. Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye.

22. Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?

23. Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.

24. Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo 1 mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.

25. Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.

26. Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

27. 4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.

28. Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, 6 Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; 7 pakuti Atate ali wamkuru ndi Ine.

Werengani mutu wathunthu Yohane 14