Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 14:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe.

12. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, nchito zimene ndicita Ine adzazicitanso iyeyu; ndipo adzacita zoposa izi; cifukwa ndipita Ine kwa Atate.

13. Ndipo cimene ciri conse mukafunse m'dzina langa, ndidzacicita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.

14. Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzacita.

15. Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.

16. Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse,

17. ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.

18. Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu.

19. Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.

20. Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 14