Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 14:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.

2. M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.

3. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.

4. Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace.

5. Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji?

6. Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

7. Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye.

8. Filipo ananena ndi iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira.

9. Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?

Werengani mutu wathunthu Yohane 14