Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 13:6-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?

7. Yesu anayankha nati kwa iye, Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwace.

8. Petro ananena ndi iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine.

9. Simoni Petro ananena ndi iye, Ambuye, si mapazi anga okha, komanse manja ndi mutu.

10. Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.

11. Pakuti anadziwa amene adzampereka iye; cifukwa ca ici anati, Simuli oyera nonse.

12. Pamenepo, atatha iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ace, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga cimene ndakucitirani inu; mucizindikira kodi?

13. Inu mundicha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.

14. Cifukwa cace, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzaceo

15. Pakuti ndakupatsani inu citsanzo, kuti, monga Ine ndakucitirani inu, inunso mucite.

16. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wace; kapena mtumwi sali wamkuru ndi womtuma iye,

17. Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzicita.

18. Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti colemba cikwaniridwe, iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine cinendene cace.

19. Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, cisadacitike, kuti pamene citacitika, mukakhulupire kuti ndine amene.

20. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene ali yense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.

Werengani mutu wathunthu Yohane 13