Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 13:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wace; kapena mtumwi sali wamkuru ndi womtuma iye,

17. Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzicita.

18. Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti colemba cikwaniridwe, iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine cinendene cace.

19. Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, cisadacitike, kuti pamene citacitika, mukakhulupire kuti ndine amene.

20. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene ali yense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.

21. Yesu m'mene adanenaizi, anabvutika mumzimu, nacita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.

22. Akuphunzira analikupenyanawina kwa mnzace, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani.

23. Koma mmodzi wa akuphunzira ace, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa cifuwa ca Yesu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 13