Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 13:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma pasanafike phwando la Paskha, Yesu, podziwa kuti nthawi yace idadza yakucoka kuturuka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ace a iye yekha a m'dziko lapansi, anawakomia kufikira cimariziro.

2. Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adathakuika mu mtima wace wa Yudase mwana wa Simoni Isikariote, kuti akampereke iye,

3. Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa iye zonse m'manja mwace, ndi kuti anacokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,

4. ananyamuka pamgonero, nabvula malaya ace; ndipo m'mene adatenga copukutira, anadzimanga m'cuuno.

5. Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ace, ndi kuwapukuta ndi copukutira, cimene anadzimanga naco,

6. Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?

7. Yesu anayankha nati kwa iye, Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwace.

8. Petro ananena ndi iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine.

9. Simoni Petro ananena ndi iye, Ambuye, si mapazi anga okha, komanse manja ndi mutu.

10. Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.

11. Pakuti anadziwa amene adzampereka iye; cifukwa ca ici anati, Simuli oyera nonse.

12. Pamenepo, atatha iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ace, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga cimene ndakucitirani inu; mucizindikira kodi?

Werengani mutu wathunthu Yohane 13