Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 12:22-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Filipo anadza nanena kwa Andreya; nadza Andreya ndi Filipo, nanena ndi Yesu.

23. Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.

24. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala cipatso cambiri.

25. Iye wokonda moyo wace adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wace m'dziko lino lapansi adzausungira ku moyo wosatha.

26. Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga, Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamcitira ulemu iyeyu,

27. Moyo wanga wabvutika tsopano; ndipo ndidzanena ciani? Atate, ndipulumutseni Ine ku nthawi iyi. Koma cifukwa ca ici ndinadzera nthawi iyi.

28. Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ocokera Kumwamba, ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.

29. Cifukwa cace khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi iye.

30. Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika cifukwa ca Ine, koma ca inu.

31. Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano,

32. Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha.

Werengani mutu wathunthu Yohane 12