Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 12:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi iye, m'mene anaitana Lazaro kuturuka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anacita umboni.

18. Cifukwa ca icinso khamulo linadza kudzakomana ndi iye, cifukwa anamva kuti iye adacita cizindikilo ici.

19. Cifukwa cace Afarisi ananena wina ndi mnzace, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pace pa iye.

20. Koma panali Ahelene ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira paphwando,

21. Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa m'Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.

22. Filipo anadza nanena kwa Andreya; nadza Andreya ndi Filipo, nanena ndi Yesu.

23. Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.

24. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala cipatso cambiri.

25. Iye wokonda moyo wace adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wace m'dziko lino lapansi adzausungira ku moyo wosatha.

Werengani mutu wathunthu Yohane 12