Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 12:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Usaope, mwana wamkazi wa Ziyoni; taona Mfumu yako idza wokhala pa mwana wa buru.

16. Izisanazidziwa aku phunzira ace poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukila kuti izi zinalembedwa za iye, ndi kuti adamcitira iye izi.

17. Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi iye, m'mene anaitana Lazaro kuturuka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anacita umboni.

18. Cifukwa ca icinso khamulo linadza kudzakomana ndi iye, cifukwa anamva kuti iye adacita cizindikilo ici.

19. Cifukwa cace Afarisi ananena wina ndi mnzace, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pace pa iye.

20. Koma panali Ahelene ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira paphwando,

Werengani mutu wathunthu Yohane 12