Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 11:42-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma cifukwa ca khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ici, kuti akhulupire kuti Inu munandituma Ine.

43. Ndipom'mene adanena izi, ana pfuula ndi mau akuru, Lazaro, turuka.

44. Ndipo womwalirayo anaturuka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yace inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.

45. Cifukwa cace ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Mariya, m'mene anaona cimene anacita, anakhulupirira iye.

46. Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazicita.

47. Pamenepo ansembe akulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? cifukwa munthu uyu acita zizindikilo zambiri.

48. Ngati timleka iye kotero, onse adzakhulupirira iye; ndipo adzadza Aroma nadzacotsa malo athu ndi mtundu wathu.

49. Koma wina mmodzi wa mwa iwo, Kayafa, wokhaia mkulu wa ansembe caka comweco anati kwa iwo, Simudziwa kanthu konse inu,

50. kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke,

51. Koma ici sananena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe caka comweco ananenera kuti Yesu akadzafera mtunduwo;

52. ndipo si cifukwa ca mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo.

53. Cifukwa cace, kuyambira tsiku Iomwelo anapangana kuti amuphe iye.

54. Cifukwa cace Yesu sanayandeyendanso poonekera mwa Ayuda, koma anacokapo kunka ku dziko loyandikira cipululu, kumudzi dzina lace Efraimu; nakhala komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.

55. Koma Paskha wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kucoka ku miraga, usanafike Paskha, kukadziyeretsa iwo okha.

56. Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzace poimirira iwo m'Kacisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuphwando kodi?

57. Koma ansembe akulu ndi Afarisi adalamulira, kuti, munthu wina akadziwa pokhala iye, aulule, kuti akamgwire iye.

Werengani mutu wathunthu Yohane 11