Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 11:4-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma cifukwa ca ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.

5. Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wace, ndi Lazaro.

6. Cifukwa cace pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri.

7. Ndipo pambuyo pace ananena kwa akuphunzira ace, Tiyeni tipitenso ku Yudeya.

8. Akuphunzira ananena ndi iye, Ambuye, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?

9. Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, cifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi,

10. Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, cifukwa mulibe kuunika mwa iye.

11. Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo tace.

12. Cifukwa cace akuphunzira ace anati kwa iye, Ambuye, ngati ali m'tulo adzacira.

13. Koma Yesu adanena za imfa yace; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.

14. Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.

15. Ndipo ndikondwera cifukwa ca inu kuti kunalibe Ine komweko, cakuti mukakhulupire; koma tiyeni, tipite kwa iye.

16. Pamenepo Tomasi, wochedwa Didimo, anati kwa akuphunzira anzace, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.

17. Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai.

18. Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yace yonga ya mastadiya khumi ndi asanu;

19. koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.

20. Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi iye; koma Mariya anakhalabe m'nyumba.

Werengani mutu wathunthu Yohane 11