Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 11:38-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.

39. Yesu ananena, Cotsani mwala. Marita, mlongo wace wa womwalirayo, ananena ndi iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.

40. Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero wa Mulungu?

41. Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.

42. Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma cifukwa ca khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ici, kuti akhulupire kuti Inu munandituma Ine.

43. Ndipom'mene adanena izi, ana pfuula ndi mau akuru, Lazaro, turuka.

44. Ndipo womwalirayo anaturuka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yace inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.

45. Cifukwa cace ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Mariya, m'mene anaona cimene anacita, anakhulupirira iye.

46. Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazicita.

Werengani mutu wathunthu Yohane 11