Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 11:31-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.

32. Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.

33. Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika mwini,

34. nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni, mukaone.

35. Yesu analira.

36. Cifukwa cace Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi!

37. Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sanakhoza kodi kucita kuti sakadafa ameneyunso?

38. Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.

39. Yesu ananena, Cotsani mwala. Marita, mlongo wace wa womwalirayo, ananena ndi iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.

40. Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero wa Mulungu?

41. Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.

42. Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma cifukwa ca khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ici, kuti akhulupire kuti Inu munandituma Ine.

43. Ndipom'mene adanena izi, ana pfuula ndi mau akuru, Lazaro, turuka.

Werengani mutu wathunthu Yohane 11