Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 11:15-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo ndikondwera cifukwa ca inu kuti kunalibe Ine komweko, cakuti mukakhulupire; koma tiyeni, tipite kwa iye.

16. Pamenepo Tomasi, wochedwa Didimo, anati kwa akuphunzira anzace, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.

17. Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai.

18. Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yace yonga ya mastadiya khumi ndi asanu;

19. koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.

20. Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi iye; koma Mariya anakhalabe m'nyumba.

21. Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.

22. Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu.

23. Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka.

24. Marita ananena ndi iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomariza.

25. Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;

26. ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ici?

27. Ananena ndi iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.

28. Ndipo m'mene anati ici anacoka naitana Mariya mbale wace m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.

29. Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa iye.

30. (Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye)

31. Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.

32. Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.

Werengani mutu wathunthu Yohane 11