Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 11:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Mariya ndi mbale wace Marita.

2. Koma ndiye Mariya uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ace ndi tsitsi lace, amene mlongo wace Lazaro anadwala.

3. Pamenepo alongo ace anatumiza kwa iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.

4. Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma cifukwa ca ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.

5. Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wace, ndi Lazaro.

6. Cifukwa cace pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri.

Werengani mutu wathunthu Yohane 11