33. Ayuda anamyankha iye, Cifukwa ca nchito yabwino sitikuponyani miyala, koma cifukwa ca mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu,
34. Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'cilamulo canu, Ndinati Ine, Muli milungu?
35. Ngati anawacha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo colemba sicingathe kutyoka),
36. kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma ku dziko lapansi, Ucita mwano; cifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?
37. Ngati sindicita nchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine.
38. Koma ngati ndicita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani nchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi ine mwa Atate.
39. Anafunanso kumgwira iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao.
40. Ndipo anacoka kunkanso tsidya lija la Yordano, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.
41. Ndipo ambiri anadza kwa iye; nanena kuti, Sanacita cizindikilo Yohane; koma zinthu ziri zonse Yohane ananena za iye zinali zoona.
42. Ndipo ambiri anakhulupirira iye komweko.