Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 10:17-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Cifukwa ca ici Atate andikonda Ine, cifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso,

18. Palibe wina andicotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndiri nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndiri nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa. Atate wanga.

19. Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda cifukwa ca mau awa.

20. Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi ciwanda, nacita misala; mukumva iye bwanji?

21. Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa ciwanda. Kodi ciwanda cikhoza kumtsegulira maso wosaona?

22. Koma kunali phwando la kukonzersanso m'Yerusalemu; nyengoyo ndi yacisanu.

23. Ndipo Yesu analikuyendayenda m'Kacisi m'khumbi la Solomo,

24. Pamenepo Ayuda anamzungulira iye, nanena ndi iye, Kufikira liti musfnkhitsa-slnkhitsa moyo wathu? ngati Inu ndinu Kristu, tiuzeni momveka.

25. Yesu anayankha iwo, Ndakuuzani, ndipo simukhulupirira, Nchitozi ndizicita Ine m'dzina la Atate wanga, zimenezi zindicitira umboni.

26. Koma inu simukhulupira, cifukwa simuli a mwa nkhosa zanga.

27. Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.

28. Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka ku nthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa,

29. Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m'dzanja la Atate.

30. Ine ndi Atate ndife amodzi.

Werengani mutu wathunthu Yohane 10