Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 1:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira.

6. Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lace ndiye Yohane.

7. Iyeyu anadza mwa umboni kudzacita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye,

8. iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukacita umboni wa kuunikaku.

9. Uku ndiko kuunika kweni kweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.

10. Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi iye, koma dziko silinamzindikira iye.

11. Anadza kwa zace za iye yekha, ndipo ace a mwini yekha sanamlandira iye.

12. Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace;

13. amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi cifuniro ca thupi, kapena ndi cifuniro ca munthu, koma ca Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 1