Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 1:48-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

48. Natanayeli ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.

49. Natanayeli anayankha Iye, Rabi, 14 Inu ndinu Mwana wa Mulungu, 15 ndinu Mfumu ya Israyeli,

50. Yesu anayankha nati kwa iye, Cifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? udzaona zoposa izi.

51. Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi Inu, 16 Mudzaona thambo lotseguka, ndi angeloa Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa munthu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 1