Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 1:25-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Kristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?

26. Yohane anawayankha, nati, 2 Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa,

27. 3 ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira lamba la nsapato yace.

28. Zinthu izi zinacitika m'Betaniya tsidya lija la Y ordano, pomwe analikubatiza Yohane.

29. M'mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, 4 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu 5 amene acotsa cimo lace la dziko lapasi!

30. 6 Ndiye amene ndinati za iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.

31. Ndipo sindinamdziwa iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israyeli, 7 cifukwa ca ici ndinadzaine kudzabatiza ndi madzi.

32. Ndipo Yohane anacita umboni, nati, 8 Ndinaona Mzimu alikutsika kucokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa iye.

33. Ndipo sindinamdziwa iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa iye, 9 yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.

Werengani mutu wathunthu Yohane 1