Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 5:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nanga tsono acuma inu, lirani ndi kucema cifukwa ca masautso anu akudza pa inu,

2. Cuma canu caola ndi zobvala zanu zajiwa ndi njenjete.

3. Golidi wanu ndi siliva wanu zacita dzimbiri, ndipo dzimbiri lace lidzacita mboni zoneneza Inu ndipo zidzadya nyama yanu ngat: moto. Mwadzikundikira cuma masiku otsiriza.

4. Taonani, mphotho ya anchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ipfuula; ndipo mapfuulc a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.

5. Mwadyerera padziko, ndipo mwacita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m'tsiku lakupha.

6. Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakanizainu.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 5