Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 4:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena cabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kucita nsanje?

6. Koma apatsa cisomo coposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.

7. Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

8. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.

9. Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi cimwemwe canu cisanduke cisoni.

10. Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

11. Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wace, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suliwocita lamulo, komatu woweruza.

12. Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?

Werengani mutu wathunthu Yakobo 4