Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 4:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mudzi wakuti wakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, Ddi kupindula nao;

14. inu amene simudziwa cimene cidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.

15. Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzacita kakuti kakuti.

16. Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kuli konse kotero nkoipa.

17. Potero kwa iye amene adziwa kucita bwino, ndipo sacita, kwa iye kuli cimo.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 4