Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 4:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

11. Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wace, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suliwocita lamulo, komatu woweruza.

12. Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?

13. Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mudzi wakuti wakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, Ddi kupindula nao;

14. inu amene simudziwa cimene cidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.

15. Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzacita kakuti kakuti.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 4