Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 4:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zicokera kuti nkhondo, zicokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizicokera ku zikhumbitso zanu zocita nkhondo m'ziwalo zanu?

2. Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimucita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimucita nkhondo; mulibe kanthu, cifukwa simupempha.

3. Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukacimwaze pocita zikhumbitso zanu.

4. Akazi acigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uti udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.

5. Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena cabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kucita nsanje?

6. Koma apatsa cisomo coposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.

7. Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

8. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.

9. Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi cimwemwe canu cisanduke cisoni.

10. Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

11. Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wace, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suliwocita lamulo, komatu woweruza.

12. Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?

13. Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mudzi wakuti wakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, Ddi kupindula nao;

Werengani mutu wathunthu Yakobo 4