Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 3:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Kotero lilimenso liri ciwalo cacing'ono, ndipo lidzikuzira zazikuru, Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri!

6. Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la cosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a cibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi gehena.

7. Pakuti mtundu uli wonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;

8. koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; liri coipa cotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.

9. Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;

10. mocokera m'kamwa momwemo muturuka ciyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.

11. Kodi kasupe aturutsira pa una womwewo madzi okoma ndi owawa?

12. Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amcere sakhoza kuturutsa okoma.

13. Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ace abwino nchito zace mu nzeru yofatsa.

14. Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi cotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana naco coonadi.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 3