Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 3:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

3. Koma ngati tiikiraakavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao Ionse,

4. Taonani, zombonso, zingakhale zazikuru zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kuli konse afuna wogwira tsigiro.

5. Kotero lilimenso liri ciwalo cacing'ono, ndipo lidzikuzira zazikuru, Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri!

6. Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la cosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a cibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi gehena.

7. Pakuti mtundu uli wonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;

8. koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; liri coipa cotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 3