Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 3:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ace abwino nchito zace mu nzeru yofatsa.

14. Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi cotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana naco coonadi.

15. Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu iri ya padziko, ya cifuniro ca cibadwidwe, ya ziwanda.

16. Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali cisokonekero ndi cocita coipa ciri conse.

17. Koma nzeru yocokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala cifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.

18. Ndipo cipatso ca cilungamo cifesedwa mumtendere kwa iwo akucita mtendere.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 3