Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 2:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma ngati mucita cikwanirire lamulolo lacifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, mucita bwino:

9. koma ngati musamala maonekedwe, mucita ucimo, ndipo mutsutsidwa ndi cilamulo monga olakwa.

10. Pakuti amene ali yense angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wacimwira onse.

11. Pakuti Iye wakuti, Usacite cigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kucita cigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

12. Lankhulani motero, ndipo citani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.

13. Pakuti ciweruziro ciribe cifundo kwa iye amene sanacita cifundo; cifundo cidzitamandira kutsutsana naco ciweruziro.

14. Cipindulocace nciani, abale anga, munthu akanena, Ndiri naco cikhulupiriro, koma alibe nchito? Kodi cikhulupiriroco cikhoza kumpulumutsa?

Werengani mutu wathunthu Yakobo 2