Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 2:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Abate anga, musakhale naco cikhulupiriro ca Ambuye wathu Yesu Kristu, Ambuye wa ulemerero, ndi kusamala maonekedwe.

2. Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wobvala mphete yagolidi, ndi cobvala cokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi cobvala codetsa:

3. ndipo mukapenyerera iye wobvala cokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, ima uko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;

4. kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?

5. Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi cikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonieza kwa iwo akumkonda iye?

6. Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu acuma, nakukokerani iwowa ku mabwalo a mirandu?

7. Kodi sacitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?

8. Koma ngati mucita cikwanirire lamulolo lacifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, mucita bwino:

Werengani mutu wathunthu Yakobo 2