Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. YAKOBO, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Kristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'cibalaliko: ndikulankhulani.

2. Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundu mitundu;

3. pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro.

4. Koma cipiriro cikhale nayo nchito yace yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda cirema, osasowa kanthu konse.

5. Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,

6. Koma apemphe ndi cikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.

7. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye;

Werengani mutu wathunthu Yakobo 1