1. YAKOBO, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Kristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'cibalaliko: ndikulankhulani.
2. Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundu mitundu;
3. pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro.
4. Koma cipiriro cikhale nayo nchito yace yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda cirema, osasowa kanthu konse.