Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Tito 3:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha.

8. Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a nchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;

9. koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndeu, ndi makani a pamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo ziri zacabe.

10. Munthu wopatukira cikhulupiriro, utamcenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize,

11. podziwa kuti worereyo wasandulika konse, nacimwa, nakhala wodzitsutsa Yekha.

12. Pamene ndikatuma Artema kwa iwe, kapena Tukiko, cita cangu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yacisanu.

13. Zena nkhoswe ya mirandu, ndi Apolo ufulumire kuwakonzera zaulendo, kuti asasowe kanthu,

14. Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge nchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipstso.

15. Akulankhula iwe onse akukhala pamodzi ndi ine. Lankhula otikondawo m'cikhulupiriro.Cisomo cikhale ndi inu nonse.

Werengani mutu wathunthu Tito 3