Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Tito 2:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'cikhulupiriro, m'cikondi, m'cipiriro.

3. Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa naco cikondi ca pavinyo, akuphunzitsa zokoma;

4. kuti akalangize akazi ang one akonde amuna ao, akonde ana ao,

5. akhale odziletsa, odekha, ocita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angacitidwe mwano.

6. Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa;

7. m'zonse udzionetsere wekha citsanzo ca nchito zabwino; m'ciphunzitse cako uonetsere cosabvunda, ulemekezeko,

8. mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana acite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.

9. Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m'zonse; osakana mau ao;

10. osatapa pa zao, komatu aonetsere cikhulupiriko conse cabwino; kuti akakometsere ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.

11. Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse,

12. ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

Werengani mutu wathunthu Tito 2