Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mateyu 28:7-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ace, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.

8. Ndipo iwo anacoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukuru, nathamanga kukauza ophunzira ace.

9. Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ace, namgwadira.

10. Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.

11. Ndipo pameneiwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe akuru zonse zimene zinacitidwa.

12. Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akuru, anakhala upo, napatsa asilikariwo ndalama zambiri,

13. nati, Kazinenani, kuti ophunzira ace anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo.

14. Ndipo ngati ici cidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa.

15. Ndipo iwo analandira ndalamazo, nacita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.

16. Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangifa.

17. Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.

18. Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.

19. Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

Werengani mutu wathunthu Mateyu 28