Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mateyu 28:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akuru, anakhala upo, napatsa asilikariwo ndalama zambiri,

13. nati, Kazinenani, kuti ophunzira ace anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo.

14. Ndipo ngati ici cidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa.

15. Ndipo iwo analandira ndalamazo, nacita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.

16. Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangifa.

17. Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.

18. Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.

19. Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

20. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya pansi pano.

Werengani mutu wathunthu Mateyu 28