1. Ndipo popita dzuwa la Sabata, mbanda kuca, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Mariya wa Magadala, ndi Mariya winayo, kudzaona manda.
2. Ndipo onani, panali cibvomezi cacikuru; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pace.
3. Kuonekera kwace kunali ngati mphezi, ndi cobvala cace coyeretsa ngati matalala;
4. ndipo ndi kuopsa kwace alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa.
5. Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapacikidwa.
6. Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.
7. Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ace, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.
8. Ndipo iwo anacoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukuru, nathamanga kukauza ophunzira ace.