Nanga muyesa bwanji? ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu manu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?