Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 9:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.

5. Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.

6. Pakuti sanadziwa cimene adzayankha; cifukwa anacita mantha ndithu.

7. Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munaturuka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.

8. Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.

9. Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamulira kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pamene Mwana wa munthu akadzauka kwa akufa ndipo.

10. Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nciani?

11. Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya?

12. Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa cabe?

13. Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamcitiranso ziri zonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.

14. Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikuru la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.

15. Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlankhula.

16. Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsa na nao ciani?

Werengani mutu wathunthu Marko 9