Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 9:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya?

12. Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa cabe?

13. Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamcitiranso ziri zonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.

14. Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikuru la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.

15. Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlankhula.

16. Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsa na nao ciani?

17. Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula;

18. ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo acita thobvu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti auturutse; koma sanakhoza.

19. Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.

Werengani mutu wathunthu Marko 9