Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 8:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nacoka kunka ku tsidya lija.

14. Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m'ngalawa koma umodzi wokha.

15. Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi, ndi cotupitsa mkate ca Herode.

16. Ndipo anatsutsana wina ndi mnzace, nanena kuti, Tiribe mikate.

17. Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana cifukwa mulibe mkate? kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? kodi muli nayo mitima yanu youma?

18. Pokhala nao maso simupenya kodi? ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? ndipo simukumbukila kodi?

19. Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri.

Werengani mutu wathunthu Marko 8