Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 7:24-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo Iye anauka nacoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Turo ndi Sidoni, Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoza kubisika.

25. Koma pomwepo mkazi, kabuthu kace kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ace.

26. Koma mkaziyo anali Mhelene, mtundu wace MsuroFonika. Ndipo anampempha Iye kuti aturutse ciwanda m'mwana wace.

27. Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana ndi kuutayira tiagaru,

28. Koma iye anabvomera nanena ndi Iye, inde Ambuye; tingakhale tiagaru ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.

29. Ndipo anati kwa iye, Cifukwa ca mau amene, muka; ciwanda caturuka m'mwana wako wamkazi.

30. Ndipo anacoka kunka kunyumba kwace, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi ciwanda citaturuka.

Werengani mutu wathunthu Marko 7