Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 7:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pakuti m'kati mwace mwa mitima ya anthu, muturuka maganizo oipa, zaciwerewere,

22. zakuba, zakupha, zacigololo, masiriro, zoipa, cinyengo, cinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:

23. zoipa izi zonse zituruka m'kati, nizidetsa munthu.

24. Ndipo Iye anauka nacoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Turo ndi Sidoni, Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoza kubisika.

25. Koma pomwepo mkazi, kabuthu kace kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ace.

26. Koma mkaziyo anali Mhelene, mtundu wace MsuroFonika. Ndipo anampempha Iye kuti aturutse ciwanda m'mwana wace.

27. Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana ndi kuutayira tiagaru,

28. Koma iye anabvomera nanena ndi Iye, inde Ambuye; tingakhale tiagaru ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.

29. Ndipo anati kwa iye, Cifukwa ca mau amene, muka; ciwanda caturuka m'mwana wako wamkazi.

Werengani mutu wathunthu Marko 7