Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 7:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo iye wakunenera zotpa atate wace kapena amai wace, afe ndithu;

11. koma inu munena, Munthu akati kwa atate wace, kapena amai wace, Karban, ndiko kuti Mtulo, cimene ukadathandizidwa naco ndi ine,

12. simulolanso kumcitira kanthu atate wace kapena amai wace;

13. muyesa acabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzicita.

14. Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:

15. kulibe kanthu kunja kwa munthu kakulowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakuturuka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.[

16. ]

17. Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ace anamfunsa Iye faruzolo.

18. Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kali konse kocokera kunja kakulowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;

19. cifukwa sikalowa mumtima mwace, koma m'mimba mwace, ndipo katurukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.

Werengani mutu wathunthu Marko 7