Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 7:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akucokera ku Yerusalemu,

2. ndipo anaona kuti ophunzira ace ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.

3. Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akuru;

4. ndipo pakucoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo ziripo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.

5. Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akuru, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?

6. Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa,Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao,Koma mtima wao ukhala kutari ndi ine.

7. Koma andilambira Ine kwacabe,Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

8. Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.

9. Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu,

10. Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo iye wakunenera zotpa atate wace kapena amai wace, afe ndithu;

11. koma inu munena, Munthu akati kwa atate wace, kapena amai wace, Karban, ndiko kuti Mtulo, cimene ukadathandizidwa naco ndi ine,

12. simulolanso kumcitira kanthu atate wace kapena amai wace;

13. muyesa acabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzicita.

Werengani mutu wathunthu Marko 7