Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 6:46-56 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

46. Ndipo atalawirana nao, anacoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera,

47. Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda.

48. Ndipo pakuwaona ali kubvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa uionda wacinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;

49. koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, napfuula:

50. pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope,

51. Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m'ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukuru mwa iwo okha;

52. pakuti sanazindikira za mikateyo, kama mitima yao inauma.

53. Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakoceza padooko.

54. Ndipo pamene anaturuka m'ngalawa anamzindikila pomwepo,

55. nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwaia pa akama ao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye.

56. Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'miraga, anthu anagoneka odwala pamisika, 1 nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya cobvala cace; ndipo onse amene anamkhudza anaciritsidwa.

Werengani mutu wathunthu Marko 6