Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 6:39-55 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulu magulu pamsipu.

40. Ndipo anakhala pansi mabungwe mabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu.

41. Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'anakumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.

42. Ndipo anadya iwo onse, nakhuta.

43. Ndipo anatola makombo mitanga khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba.

44. Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.

45. Ndipo pomwepo Iye anakangamiza ophunzira ace alowe rri'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.

46. Ndipo atalawirana nao, anacoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera,

47. Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda.

48. Ndipo pakuwaona ali kubvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa uionda wacinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;

49. koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, napfuula:

50. pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope,

51. Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m'ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukuru mwa iwo okha;

52. pakuti sanazindikira za mikateyo, kama mitima yao inauma.

53. Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakoceza padooko.

54. Ndipo pamene anaturuka m'ngalawa anamzindikila pomwepo,

55. nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwaia pa akama ao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye.

Werengani mutu wathunthu Marko 6